Ndipo iye anachoka kumeneko kunka kuphiri la kum'mawa kwa Betele, namanga hema wake; Betele anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.
1 Samueli 30:27 - Buku Lopatulika Anatumiza kwa iwo a ku Betele, ndi kwa iwo a ku Ramoti wa kumwera, ndi kwa iwo a ku Yatiri; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anatumiza kwa iwo a ku Betele, ndi kwa iwo a ku Ramoti wa kumwera, ndi kwa iwo a ku Yatiri; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mphatsozo zidaperekedwa kwa anthu a ku Betele, a ku Ramoti kumwera kwa Yuda, a ku Yatiri, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anatumiza mphatsozo kwa anthu a ku Beteli, Ramoti-Negavi, Yatiri, |
Ndipo iye anachoka kumeneko kunka kuphiri la kum'mawa kwa Betele, namanga hema wake; Betele anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.
Ndipo gawo la ana a Yosefe linatuluka kuchokera ku Yordani ku Yeriko, ku madzi a Yeriko kum'mawa, kuchipululu, nakwera kuchokera ku Yeriko kunka kumapiri ku Betele;
ndi midzi yonse yozungulira mizinda iyi mpaka Baalati-Bere ndiwo Rama kumwera. Ndicho cholowa cha fuko la ana a Simeoni, monga mwa mabanja ao.
Ndipo Yoswa anatuma amuna kuchokera ku Yeriko apite ku Ai, ndiwo pafupi pa Betaveni, kum'mawa kwa Betele; nanena nao, Kwerani ndi kukazonda dziko. Nakwera amunawo, nazonda Ai.
Ndipo Yoswa anawatuma, namuka iwo kulowa m'molalira, nakhala pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa Ai; koma Yoswa anakhala mwa anthu usiku uja.