1 Samueli 30:21 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anatuluka kuchingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anatuluka kuchingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Davide adakafika kwa anthu 200 otopa kwambiri ndi osathanso kuyenda aja, amene adaaŵasiya ku mtsinje wa Besori. Iwo adanyamuka napita kukakumana ndi Davide ndi anthu amene anali naye aja. Davide adaŵayandikira naŵalonjera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anafika ku malo kumene kunali anthu 200 otopa kwambiri aja amene sanathe kutsagana naye koma anangokhala ku mtsinje wa Besori. Tsono ananyamuka kuti akumane ndi Davide pamodzi ndi anthu amene anali naye. Davide anawayandikira nawalonjera. |
Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;
Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Zalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna akhala m'dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema?
nunyamule nchinchi izi khumi zamase ukapatse mtsogoleri wa chikwi chao, nukaone m'mene akhalira abale ako, nulandire chikole chao.
Ndipo Davide anasiya akatundu ake m'dzanja la wosungira akatundu, nathamangira ku khamulo, nadza nawalonjera abale ake.
Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, chifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori.
Pamenepo anthu oipa onse, ndi opanda pake a iwo amene anapita ndi Davide anayankha nati, Popeza sadamuke nafe sitidzawapatsa kanthu ka zofunkha tidazilanditsa, koma kwa munthu yense mkazi wake ndi ana ake, kuti achoke nao namuke.