Anakanthanso a m'mahema a ng'ombe, nalanda nkhosa zochuluka, ndi ngamira; nabwerera kunka ku Yerusalemu.
1 Samueli 30:20 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anatenga nkhosa zonse ndi ng'ombe zonse, zimene anazipirikitsa patsogolo pa zoweta zaozao, nati, Izi ndi zofunkha za Davide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anatenga nkhosa zonse ndi ng'ombe zonse, zimene anazipirikitsa patsogolo pa zoweta zaozao, nati, Izi ndi zofunkha za Davide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adalanditsanso nkhosa zonse ndi ng'ombe zomwe. Ndipo anthu ankakusa zoŵetazo namati, “Izi ndi za Davide.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anapulumutsanso nkhosa ndi ngʼombe zonse. Tsono anthu ankakusa ziwetozo namati, “Izi ndizo zofunkha za Davide.” |
Anakanthanso a m'mahema a ng'ombe, nalanda nkhosa zochuluka, ndi ngamira; nabwerera kunka ku Yerusalemu.
Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ake kutenga zofunkha zao, anapezako chuma chambiri, ndi mitembo yambiri ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinachuluka.
Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.
Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anatuluka kuchingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji.
Ndipo pamene Davide anafika ku Zikilagi, anatumizako za zofunkhazo kwa akulu a Yuda, ndiwo abwenzi ake, nati, Siyi mphatso yanu ya zofunkha za adani a Yehova.