Kodi simunamtchinge iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m'dziko.
1 Samueli 30:19 - Buku Lopatulika Ndipo sikanasoweka kanthu, kakang'ono kapena kakakulu, ana aamuna kapena ana aakazi, kapena chuma kapena china chilichonse cha zija anazitenga iwowa; Davide anabwera nazo zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo sikanasoweka kanthu, kakang'ono kapena kakakulu, ana amuna kapena ana akazi, kapena chuma kapena china chilichonse cha zija anazitenga iwowa; Davide anabwera nazo zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Panalibe kanthu kalikonse kamene kadasoŵapo. Adalanditsa ana aamuna ndi ana aakazi, ndiponso chilichonse chimene chidaatengedwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Palibe chimene chinasowa anthu onse, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, mnyamata mpaka mtsikana anapulumutsidwa. Davide anapulumutsa chilichonse chimene anafunkha Aamaleki aja. |
Kodi simunamtchinge iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m'dziko.
nati kwa Mose, Atumiki anu anawerenga ankhondo tinali nao, ndipo sanasowe munthu mmodzi wa ife.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
Ndipo Davide anatenga nkhosa zonse ndi ng'ombe zonse, zimene anazipirikitsa patsogolo pa zoweta zaozao, nati, Izi ndi zofunkha za Davide.
Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndikalondola khamulo ndidzalipeza kodi? Ndipo anamyankha kuti, Londola, pakuti zoonadi udzawapeza, ndi kulanditsa zonse.