Ndipo anabwera nacho chuma chonse, nabwera naye Loti yemwe ndi chuma chake, ndi akazi ndi anthu omwe.
1 Samueli 30:18 - Buku Lopatulika Ndipo Davide analanditsa zonse anazitenga Aamaleke, napulumutsa akazi ake awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide analanditsa zonse anazitenga Aamaleke, napulumutsa akazi ake awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Davide adalanditsa zinthu zonse zimene adaatenga Aamaleke. Ndipo adapulumutsanso akazi ake aŵiri aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Davide analanditsa zinthu zonse zimene Aamaleki aja anatenga. Anapulumutsanso akazi ake awiri aja. |
Ndipo anabwera nacho chuma chonse, nabwera naye Loti yemwe ndi chuma chake, ndi akazi ndi anthu omwe.
anatenga anthu onse, nanka kukamenyena ndi Ismaele mwana wa Netaniya, nampeza pamadzi ambiri a mu Gibiyoni.
nati kwa Mose, Atumiki anu anawerenga ankhondo tinali nao, ndipo sanasowe munthu mmodzi wa ife.
Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndikalondola khamulo ndidzalipeza kodi? Ndipo anamyankha kuti, Londola, pakuti zoonadi udzawapeza, ndi kulanditsa zonse.