1 Samueli 30:11 - Buku Lopatulika Ndipo ena anapeza Mwejipito kuthengo, nabwera naye kwa Davide, nampatsa chakudya, nadya iye; nampatsanso madzi kumwa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ena anapeza Mwejipito kuthengo, nabwera naye kwa Davide, nampatsa chakudya, nadya iye; nampatsanso madzi kumwa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu amene anali ndi Davide, akuyenda m'njira, adapeza Mwejipito, nabwera naye kwa Davide. Tsono adampatsa buledi naadya. Adampatsanso madzi akumwa, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu amene anali ndi Davide anapeza Mwigupto mʼmunda wina ndipo anabwera naye kwa Davide. Iwo anamupatsa madzi kuti amwe ndi chakudya kuti adye. |
pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine;
Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m'dziko lake.
Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, chifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori.
nampatsanso chigamphu cha nchinchi ya nkhuyu ndi nchinchi ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wake unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya chakudya, osamwa madzi.