1 Samueli 30:10 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, chifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, chifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamodzi ndi anthu 400 adapitirira kuŵalondola Aamalekewo, koma anthu 200 amene anali atatopa, adatsalira m'mbuyo, pakuti sadathe kuwoloka mtsinje wa Besori uja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide ndi anthu ake 400 anapitirira kuwalondola Aamaleki aja. Koma anthu ena 200 anatsala popeza anatopa moti sakanatha kuwoloka mtsinje wa Besori uja. |
Ndipo Saulo ndi anthu onse amene anali naye anaunjikana pamodzi, natulukira kunkhondoko; ndipo taonani, munthu yense anakantha mnzake ndi lupanga, ndipo panali kusokonezeka kwakukulu.
Ndipo anakantha Afilisti tsiku lija kuyambira ku Mikimasi kufikira ku Ayaloni, ndipo anthu anafooka kwambiri.
Ndipo ena anapeza Mwejipito kuthengo, nabwera naye kwa Davide, nampatsa chakudya, nadya iye; nampatsanso madzi kumwa;
Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anatuluka kuchingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji.
Chomwecho Davide anamuka, iye ndi anthu mazana asanu ndi limodzi anali naye, nafika kukamtsinje Besori, pamenepo anatsala ena.