1 Samueli 3:15 - Buku Lopatulika Ndipo Samuele anagona kufikira m'mawa, natsegula zitseko za nyumba ya Yehova. Ndipo Samuele anaopa kudziwitsa Eli masomphenyawo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Samuele anagona kufikira m'mawa, natsegula zitseko za nyumba ya Yehova. Ndipo Samuele anaopa kudziwitsa Eli masomphenyawo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Samuele adagona mpaka m'maŵa. Atadzuka adatsekula zitseko za nyumba ya Chauta. Ankachita mantha kumuuza Eli zimene Chauta adaamuululirazo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Samueli anagona mpaka mmawa. Atadzuka anatsekula zitseko za Nyumba ya Yehova. Iye anachita mantha kumuwuza Eli za masomphenya ake. |
Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto chabe paguwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m'dzanja lanu.
Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.
Chomwecho Hana anauka atadya mu Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wake pa mphuthu ya Kachisi wa Yehova.
Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samuele, Samuele. Pompo Samuele anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva.