Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.
1 Samueli 29:5 - Buku Lopatulika Uyu si Davide kodi amene anamthirirana mang'ombe m'magulu ao, kuti, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Uyu si Davide kodi amene anamthirirana mang'ombe m'magulu ao, kuti, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ameneyutu ndi Davide, yemwe uja ankamuvinira ndi kumuimbira kuti, “ ‘Saulo wapha zikwi inde, koma Davide wapha zikwi khumikhumi?’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Paja ameneyu ndi Davide yemwe ankamuvinira namuyimbira kuti, “ ‘Sauli wapha anthu 1,000 koma Davide wapha miyandamiyanda?’ ” |
Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.
Yemwe adalitsa mnzake ndi mau aakulu pouka mamawa, anthu adzachiyesa chimenecho temberero.
Ndipo anyamata a Akisi ananena naye, Uyu si Davide mfumu ya dzikolo kodi? Sanathirirana mang'ombe za iye kodi m'magule ao, ndi kuti, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani?