Ena a Manase omwe anapatukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Saulo, koma sanawathandize; popeza akalonga a Afilisti, atachita upo, anamuuza achoke, ndi kuti, Adzapatukira kwa mbuye wake Saulo ndi kutisandulikira.
1 Samueli 29:2 - Buku Lopatulika Ndipo akalonga a Afilisti ananyamuka ndi mazana ao ndi zikwi zao; ndipo Davide ndi anthu ake ananyamuka ndi a pambuyo pamodzi ndi Akisi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akalonga a Afilisti ananyamuka ndi mazana ao ndi zikwi zao; ndipo Davide ndi anthu ake ananyamuka ndi a pambuyo pamodzi ndi Akisi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene atsogoleri ankhondo a Afilisti ankatsogoza magulu ao a ankhondo mazana angapo ndiponso zikwi zingapo, Davide ndi ankhondo ake ankayenda pambuyo ndi Akisi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene atsogoleri a Afilisti ankatsogolera magulu awo ankhondo a miyandamiyanda, Davide ndi ankhondo ake ankayenda pambuyo pamodzi ndi Akisi. |
Ena a Manase omwe anapatukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Saulo, koma sanawathandize; popeza akalonga a Afilisti, atachita upo, anamuuza achoke, ndi kuti, Adzapatukira kwa mbuye wake Saulo ndi kutisandulikira.
Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Ahiyezere mwana wa Amisadai.
kuyambira Sihori wokhala chakuno cha Ejipito mpaka malire a Ekeroni kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asikeloni, a ku Gati, ndi a ku Ekiro, ndi Avimu;
Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yopalamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolide, ndi mbewa zisanu zagolide, monga mwa chiwerengo cha mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu.