Ndipo mfumu ya Israele inanena ndi Yehosafati, Ine ndidzadzizimbaitsa, ndi kulowa kunkhondo, koma vala iwe zovala zako zachifumu. Ndipo mfumu ya Israele inadzizimbaitsa, nilowa kunkhondo.
1 Samueli 28:8 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo anadzizimbaitsa navala zovala zina, nanka iye pamodzi ndi anthu ena awiri, nafika kwa mkaziyo usiku; nati iye, Undilotere ndi mzimu wobwebwetawo, nundiukitsire aliyense ndidzakutchulira dzina lake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo anadzizimbaitsa navala zovala zina, nanka iye pamodzi ndi anthu ena awiri, nafika kwa mkaziyo usiku; nati iye, Undilotere ndi mzimu wobwebwetawo, nundiukitsire aliyense ndidzakutchulira dzina lake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Saulo adadzizimbaitsa, navala zovala zachilendo, napita. Pamodzi ndi anthu aŵiri adakafika kwa mkaziyo usiku. Ndipo adamuuza kuti, “Undifunsire zam'tsogolo kwa mizimu, makamaka undiitanire mzimu wa amene ndimtchule.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero Sauli anadzizimbayitsa navala zovala zachilendo. Tsono iye pamodzi ndi anthu awiri anapita nakafika kwa mkazi uja usiku, ndipo anamupempha kuti, “Chonde ndifunsireni nzeru kwa mizimu ya anthu akufa. Koma makamaka munditulutsire mzimu wa amene ndimutchule.” |
Ndipo mfumu ya Israele inanena ndi Yehosafati, Ine ndidzadzizimbaitsa, ndi kulowa kunkhondo, koma vala iwe zovala zako zachifumu. Ndipo mfumu ya Israele inadzizimbaitsa, nilowa kunkhondo.
Ndipo munthu anakoka uta wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israele pakati pa maluma a malaya achitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa galeta wake, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kunkhondo, popeza ndalasidwa.
Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta, kufunsirako,
Ndi mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Ndidzadzizimbaitsa ndi kulowa kunkhondo, koma inu valani zovala zanu. Nidzizimbaitsa mfumu ya Israele, namuka iwo kunkhondo.
Koma Yosiya sanatembenuke nkhope yake kumleka, koma anadzizimbaitsa kuti ayambane naye, osamvera mau a Neko ochokera m'kamwa mwa Mulungu; nadza kuyambana naye m'chigwa cha Megido.
Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?
Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.
Pamaso pao uwasenze paphewa pako, ndi kuwatulutsa kuli mdima, nuphimbe nkhope yako kuti usapenye dziko; popeza ndakuika chizindikiro cha nyumba ya Israele.
Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza kudziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zao zinali zoipa.