Ndipo mkaziyo anali ndi mwanawang'ombe wonenepa m'nyumbamo; ndipo anafulumira, namupha, natenga ufa naukanyanga mkate wopanda chotupitsa;
1 Samueli 28:25 - Buku Lopatulika nabwera nazo kwa Saulo ndi kwa anyamata ake; nadya iwowa. Atatero ananyamuka, nachoka usiku womwewo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nabwera nazo kwa Saulo ndi kwa anyamata ake; nadya iwowa. Atatero ananyamuka, nachoka usiku womwewo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adadzapereka bulediyo kwa Saulo ndi nduna zake, ndipo onse adadya. Pambuyo pake adanyamuka, nachokapo usiku womwewo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono anapereka bulediyo kwa Sauli ndi nduna zake ndipo anadya. Pambuyo pake ananyamuka kupita kwawo usiku womwewo. |
Ndipo mkaziyo anali ndi mwanawang'ombe wonenepa m'nyumbamo; ndipo anafulumira, namupha, natenga ufa naukanyanga mkate wopanda chotupitsa;
Tsono Afilisti anasonkhanitsa makamu ao onse ku Afeki; ndipo Aisraele anamanga ku chitsime cha mu Yezireele.