Ndipo mkaziyo anafika kwa Saulo, naona kuti ali wovutika kwambiri, nanena naye, Onani, mdzakazi wanu anamvera mau anu, ndipo ndinataya moyo wanga, ndi kumvera mau anu munalankhula ndi ine.
1 Samueli 28:22 - Buku Lopatulika Chifukwa chake tsono, mumverenso mau a mdzakazi wanu, nimundilole kuika kakudya pamaso panu; ndipo mudye, kuti mukhale ndi mphamvu pakumuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake tsono, mumverenso mau a mdzakazi wanu, nimundilole kuika kakudya pamaso panu; ndipo mudye, kuti mukhale ndi mphamvu pakumuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake tsono, inunso mumvere mau anga. Mundilole ndikuikireni kabuledi pang'ono, mudye kuti muwone nyonga zoyendera.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono inunso mumvere mawu a mdzakazi wanune. Mundilole kuti ndikupatseni ka buledi pangʼono kuti mukhale ndi mphamvu zoyendera pa ulendo wanu.” |
Ndipo mkaziyo anafika kwa Saulo, naona kuti ali wovutika kwambiri, nanena naye, Onani, mdzakazi wanu anamvera mau anu, ndipo ndinataya moyo wanga, ndi kumvera mau anu munalankhula ndi ine.
Koma iye anakana, nati, Sindifuna kudya. Koma anyamata ake, pamodzi ndi mkaziyo anamkakamiza; iye anamvera mau ao. Chomwecho anauka pansi, nakhala pakama.