Koma mtima wa mfumu ya Aramu unavutika kwambiri pa ichicho, naitana anyamata ake, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wovomerezana ndi mfumu ya Israele ndani?
1 Samueli 28:21 - Buku Lopatulika Ndipo mkaziyo anafika kwa Saulo, naona kuti ali wovutika kwambiri, nanena naye, Onani, mdzakazi wanu anamvera mau anu, ndipo ndinataya moyo wanga, ndi kumvera mau anu munalankhula ndi ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mkaziyo anafika kwa Saulo, naona kuti ali wovutika kwambiri, nanena naye, Onani, mdzakazi wanu anamvera mau anu, ndipo ndinataya moyo wanga, ndi kumvera mau anu munalankhula ndi ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo mkazi uja adasendera pafupi ndi Saulo, ndipo ataona kuti akuchita mantha, adamuuza kuti, “Taonani, mdzakazi wanune ndakumverani. Ine ndataya moyo wanga pomvera zimene munandiwuza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mkazi uja tsono anasendera kufupi ndi Sauli, ndipo ataona kuti Sauli akuchita mantha, anamuwuza kuti, “Taonani, mdzakazi wanune ndakumverani. Ndayika moyo wanga pa chiswe ndipo ndamvera zimene munandiwuza. |
Koma mtima wa mfumu ya Aramu unavutika kwambiri pa ichicho, naitana anyamata ake, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wovomerezana ndi mfumu ya Israele ndani?
Ndipo pakuona ine kuti simundipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundichitira nkhondo?
popeza iye anataya moyo wake nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anachitira Aisraele onse chipulumutso chachikulu, inu munachiona, nimunakondwera; tsono mudzachimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda chifukwa?
Pomwepo Saulo anagwa pansi tantha, naopa kwakukulu, chifukwa cha mau a Samuele; ndipo analibe mphamvu; pakuti tsiku lonse ndi usiku wake wonse anakhala osadya kanthu.
Chifukwa chake tsono, mumverenso mau a mdzakazi wanu, nimundilole kuika kakudya pamaso panu; ndipo mudye, kuti mukhale ndi mphamvu pakumuka.