Nati Yehova, Adzanyenga Ahabu ndani, kuti akwere nagwe ku Ramoti Giliyadi? Ndipo anati wina mwakuti, wina mwakuti.
1 Samueli 28:19 - Buku Lopatulika Ndiponso Yehova adzapereka Israele pamodzi ndi iwe m'dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisraele m'dzanja la Afilisti. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiponso Yehova adzapereka Israele pamodzi ndi iwe m'dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisraele m'dzanja la Afilisti. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adzakupereka iweyo pamodzi ndi Aisraele kwa Afilisti. Ndipo maŵa, iwe ndi ana ako, mudzabwera kuli ine kuno. Ndithudi, Chauta adzapereka gulu lankhondo la Aisraele kwa Afilisti.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova adzapereka ndithu iweyo pamodzi ndi Aisraeli kwa Afilisti. Ndipo mmawa iweyo ndi ana ako mudzakhala ndi ine kuno. Ndithu Yehova adzapereka gulu lankhondo la Aisraeli kwa Afilisti.” |
Nati Yehova, Adzanyenga Ahabu ndani, kuti akwere nagwe ku Ramoti Giliyadi? Ndipo anati wina mwakuti, wina mwakuti.
Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.
Taona, mawa monga nthawi ino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhale unzake mu Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.
Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.
Koma Ananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha aakulu anagwera onse akumvawo.
Pomwepo Saulo anagwa pansi tantha, naopa kwakukulu, chifukwa cha mau a Samuele; ndipo analibe mphamvu; pakuti tsiku lonse ndi usiku wake wonse anakhala osadya kanthu.