kuchotsa ufumu kunyumba ya Saulo ndi kukhazika mpando wachifumu wa Davide pa Israele ndi pa Yuda, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.
1 Samueli 28:17 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova yekha wachita monga ananena pakamwa panga; ndipo Yehova wang'amba ufumuwo, kuuchotsa m'dzanja lako, ndi kuupatsa mnansi wako, ndiye Davide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova yekha wachita monga ananena pakamwa panga; ndipo Yehova wang'amba ufumuwo, kuuchotsa m'dzanja lako, ndi kuupatsa mnansi wako, ndiye Davide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta wakuchita zomwe adakuuza kudzera mwa ine. Wakulanda ufumu, waupereka kwa wina, kwa Davide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova wakuchita zimene ananeneratu kudzera mwa ine. Yehova wachotsa ufumu mʼmanja mwako ndipo waupereka kwa mnansi wako, kwa Davide. |
kuchotsa ufumu kunyumba ya Saulo ndi kukhazika mpando wachifumu wa Davide pa Israele ndi pa Yuda, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.
Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zao; ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa.
Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama.
Ndipo tsono taona ndidziwa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndi kuti ufumu wa Israele udzakhazikika m'dzanja lako.
Ndipo Samuele ananena naye, Ndipo undifunsiranji ine, popeza Yehova anakuchokera, nasandulika mdani wako?