Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng'ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye.
1 Samueli 28:14 - Buku Lopatulika Ndipo ananena naye, Makhalidwe ake ndi otani? Nati iye, Nkhalamba ilikukwera yovala mwinjiro. Pamenepo Saulo anazindikira kuti ndi Samuele, naweramitsa nkhope yake pansi, namgwadira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena naye, Makhalidwe ake ndi otani? Nati iye, Nkhalamba ilikukwera yovala mwinjiro. Pamenepo Saulo anazindikira kuti ndi Samuele, naweramitsa nkhope yake pansi, namgwadira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Saulo adafunsa mkaziyo kuti, “Kodi maonekedwe a mzimuwo ngotani?” Mkaziyo adati, “Imene ikutuluka ndi nkhalamba, yavala mkanjo.” Apo Saulo adadziŵa kuti ndi Samuele ameneyo, ndipo adapereka ulemu pakuŵerama ndi kugunditsa nkhope yake pansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli anafunsa, “Kodi mzimuwo ukuoneka motani?” Mkaziyo anayankha kuti, “Amene akutuluka ndi munthu wokalamba ndipo wavala mkanjo.” Apo Sauli anadziwa kuti anali Samueli ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi. |
Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng'ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye.
Ndipo iye ananena nayo, Nanga maonekedwe ake a munthu anakwerayo kukomana nanu, nanena nanu mau awa, ndi otani?
Ndipo Eliya anagwira chofunda chake, nachipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.
Ndipo pakupotoloka Samuele kuti achoke, iye anagwira chilezi cha mwinjiro wake, ndipo chinang'ambika.
Bwino lake Davide yemwe ananyamuka, natuluka m'phangamo, nafuulira Saulo, nati, Mbuye wanga, mfumu. Ndipo pakucheuka Saulo, Davide anaweramira nkhope yake pansi, namgwadira.
Ndipo mfumuyo inanena naye, Usaope, kodi ulikona chiyani? Mkaziyo nanena ndi Saulo, Ndilikuona milungu ilikukwera kutuluka m'kati mwa dziko.