1 Samueli 28:13 - Buku Lopatulika Ndipo mfumuyo inanena naye, Usaope, kodi ulikona chiyani? Mkaziyo nanena ndi Saulo, Ndilikuona milungu ilikukwera kutuluka m'kati mwa dziko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumuyo inanena naye, Usaope, kodi ulikona chiyani? Mkaziyo nanena ndi Saulo, Ndilikuona milungu ilikukwera kutuluka m'kati mwa dziko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mfumuyo idamuuza kuti, “Usaope. Kodi ukuwona chiyani?” Mkaziyo adati, “Ndikuwona mzimu ukutuluka pansi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumuyo inamuwuza kuti, “Usaope. Kodi ukuona chiyani?” Mkaziyo anayankha kuti, “Ndikuona mzimu ukutuluka pansi.” |
Ndipo iye adzakulankhulira iwe kwa anthu; ndipo kudzatero, kuti iye adzakhala kwa iwe ngati m'kamwa, ndi iwe udzakhala kwa iye ngati Mulungu.
Ndipo mkaziyo pakuona Samuele, anafuula ndi mau aakulu; ndi mkaziyo analankhula ndi Saulo, nati, Munandinyengeranji? Popeza inu ndinu Saulo.
Ndipo ananena naye, Makhalidwe ake ndi otani? Nati iye, Nkhalamba ilikukwera yovala mwinjiro. Pamenepo Saulo anazindikira kuti ndi Samuele, naweramitsa nkhope yake pansi, namgwadira.