Ndipo panali m'mamawa, anaona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Chiyani wandichitira ine? Kodi sindinakutumikire iwe chifukwa cha Rakele? Wandinyenga ine bwanji?
1 Samueli 28:12 - Buku Lopatulika Ndipo mkaziyo pakuona Samuele, anafuula ndi mau aakulu; ndi mkaziyo analankhula ndi Saulo, nati, Munandinyengeranji? Popeza inu ndinu Saulo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mkaziyo pakuona Samuele, anafuula ndi mau akulu; ndi mkaziyo analankhula ndi Saulo, nati, Munandinyengeranji? Popeza inu ndinu Saulo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene mkaziyo adaona Samuele, adakuwa kwambiri nati, “Chifukwa chiyani mwandinyenga? Ndinu mfumu Saulo!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene mkaziyo anaona Samueli anakuwa kwambiri, nawuza Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani inu mwandipusitsa? Inu ndinu Sauli!” |
Ndipo panali m'mamawa, anaona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Chiyani wandichitira ine? Kodi sindinakutumikire iwe chifukwa cha Rakele? Wandinyenga ine bwanji?
Ndipo Yehova ananena ndi Ahiya, Taona, mkazi wa Yerobowamu akudza kukufunsa za mwana wake, popeza adwala; udzanena naye mwakutimwakuti; popeza kudzakhala pakulowa iye adzadzizimbaitsa.
Ndipo mfumuyo inanena naye, Usaope, kodi ulikona chiyani? Mkaziyo nanena ndi Saulo, Ndilikuona milungu ilikukwera kutuluka m'kati mwa dziko.
M'menemo Samuele ndipo atafa, ndipo Aisraele onse atalira maliro ake, namuika mu Rama, m'mzinda mwao. Ndipo Saulo anachotsa m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula onse.