Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?
1 Samueli 28:11 - Buku Lopatulika Pomwepo mkaziyo anati, Ndikuukitsireni yani? Nati iye, Undiukitsire Samuele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo mkaziyo anati, Ndikuukitsireni yani? Nati iye, Undiukitsire Samuele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo mkaziyo adafunsa kuti, “Kodi ndikuitanireni yani?” Saulo adati, “Itanire Samuele.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka mkaziyo anafunsa, “Ndikuyitanireni yani?” Iye anati, “Undiyitanire Samueli.” |
Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?
Ndipo Saulo anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe chilango chidzakugwera chifukwa cha chinthu ichi.
Ndipo mkaziyo pakuona Samuele, anafuula ndi mau aakulu; ndi mkaziyo analankhula ndi Saulo, nati, Munandinyengeranji? Popeza inu ndinu Saulo.
Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita.