chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.
1 Samueli 28:10 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe chilango chidzakugwera chifukwa cha chinthu ichi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe chilango chidzakugwera chifukwa cha chinthu ichi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Saulo adalonjeza mkaziyo molumbira nati, “Pali Chauta wamoyo, sudzalangidwa kaamba ka zimenezi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Sauli analonjeza mkaziyo molumbira nati, “Pali Yehova wamoyo, iweyo sudzalangidwa chifukwa cha zimenezi.” |
chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.
Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.
Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo.
Ndipo anamlumbirira iye, kuti, Chilichonse ukandipempha ndidzakupatsa, kungakhale kukugawira ufumu wanga.
Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israele, chingakhale chili m'mwana wanga Yonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.
Ndipo mkaziyo ananena naye, Onani, mudziwa chimene anachita Saulo, kuti analikha m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula; chifukwa ninji tsono mulikutchera moyo wanga msampha, kundifetsa.