Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 27:11 - Buku Lopatulika

Ndipo Davide sadasunge wamoyo mwamuna kapena mkazi, kubwera nao ku Gati; popeza adati, Kuti angatiwulule, ndi kuti, Davide anatero, ndi makhalidwe ake ndi otere, masiku onse akukhala ku dziko la Afilisti.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Davide sadasunga wamoyo mwamuna kapena mkazi, kubwera nao ku Gati; popeza adati, Kuti angatiwulule, ndi kuti, Davide anatero, ndi makhalidwe ake ndi otere, masiku onse akukhala ku dziko la Afilisti.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Davide sankasiya wamoyo, mwamuna kapena mkazi, kuwopa kuti wopulumukayo angakanene ku Gati kuti, “Davide adatichita zakutizakuti.” Davide ankachita choncho nthaŵi zonse pamene ankakhala ku dziko la Afilisti.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Davide sankasiya mwamuna kapena mkazi wamoyo kuti akafotokozere anthu a ku Gati zochitikazo kuopa kuti opulumukawo akhoza kudzanena kuti “Davide watichita zakutizakuti.” Tsono izi ndi zimene Davide ankachita pamene ankakhala mʼdziko la Afilisti.

Onani mutuwo



1 Samueli 27:11
7 Mawu Ofanana  

Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse; koma lilime lonama likhala kamphindi.


Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.


Ndipo panali atapita masiku awiri atamupha Gedaliya, anthu osadziwa,


Ndipo Davide anati kwa Abiyatara, Tsiku lija Doegi wa ku Edomu anali kumeneko, ndinadziwiratu kuti adzauzadi Saulo; ine ndinafetsa anthu onse a nyumba ya atate wako.


Ndipo Akisi anati, Waponyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameele, ndi a kumwera kwa Akeni.


Ndipo Akisi anakhulupirira Davide, nati, Anadziipitsa ndithu pakati pa anthu a Israele, chifukwa chake iye adzakhala mnyamata wanga chikhalire.


nagwira akazi ndi onse anali m'mwemo, aakulu ndi aang'ono; sanaphe mmodzi, koma anawatenga, namuka.