Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.
1 Samueli 26:22 - Buku Lopatulika Davide nayankha, nati, Tapenyani mkondo wa mfumu! Abwere mnyamata wina kuutenga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Davide nayankha, nati, Tapenyani mkondo wa mfumu! Abwere mnyamata wina kuutenga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Davide adayankha kuti, “Suwu mkondo wanu, mfumu. Tumani mmodzi mwa ankhondowo adzatenge. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anayankha kuti, “Nawu mkondo wanu, mfumu. Tumani mmodzi wa anyamata anu abwere adzatenge. |
Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.
Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalole kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.