Ndipo anamuuza Tamara, kuti, Taona, mpongozi wako akwera kunka ku Timna kuti akasenge nkhosa zake.
1 Samueli 25:4 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anamva kuchipululu kuti Nabala alinkusenga nkhosa zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anamva kuchipululu kuti Nabala alinkusenga nkhosa zake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide anali atamva kuchipululu kuja kuti Nabala akumeta nkhosa zake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anamva akanali ku chipululu kuti Nabala akumeta nkhosa. |
Ndipo anamuuza Tamara, kuti, Taona, mpongozi wako akwera kunka ku Timna kuti akasenge nkhosa zake.
Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali nao osenga nkhosa zake ku Baala-Hazori pafupi pa Efuremu; ndipo Abisalomu anaitana ana aamuna onse a mfumu.
Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wake ndiye Abigaile; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake; ndipo iye anali wa banja la Kalebe.
Davide natuma anyamata khumi, nanena kwa anyamatawo, Mukwere ku Karimele, mumuke kwa Nabala ndi kundiperekera moni;