Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleze iwe kuti umkhudze mkaziyo.
1 Samueli 25:34 - Buku Lopatulika Pakuti ndithu, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene anandiletsa lero kusapweteka iwe, ukadapanda kufulumira kubwera kundichingamira, zoonadi sindikadasiyira Nabala kufikira kutacha kanthu konse, ngakhale mwana wamwamuna mmodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ndithu, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene anandiletsa lero kusapweteka iwe, ukadapanda kufulumira kubwera kundichingamira, zoonadi sindikadasiyira Nabala kufikira kutacha kanthu konse, ngakhale mwana wamwamuna mmodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta, Mulungu wa Israele, ndiye wandiletsa kuti ndisakupwetekeni. Zoonadi, pali Chauta, Mulungu wamoyo, mukadapanda kudzakumana nane msanga, ndithu sipakadamtsalira Nabala munthu wamwamuna ndi mmodzi yemwe maŵa m'maŵa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kunena zoona, pali Yehova Wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene wandiletsa kuti ndisakupwetekeni, mukanapanda kubwera msanga kudzakumana nane, palibe munthu aliyense wamwamuna wa Nabala akanasiyidwa wamoyo pakucha mmawa.” |
Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleze iwe kuti umkhudze mkaziyo.
Ndipo amuna a ku Gibiyoni anatumira Yoswa mau kuchigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.
Ndipo m'mawa mwake Saulo anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo mu ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri.
Pomwepo Abigaile anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zowotchaotcha, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi nchinchi za mphesa zouma zana limodzi, ndi nchinchi za nkhuyu mazana awiri, naziika pa abulu.
Mulungu alange adani a Davide, ndi kuonjezerapo, ngati ndisiyapo kufikira kuunika kwa m'mawa, kanthu konse ka iye, kangakhale kamwana kamphongo.
Chifukwa chake tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera chilango ndi dzanja la inu nokha, chifukwa chake adani anu, ndi iwo akufuna kuchitira mbuye wanga choipa, akhale ngati Nabala.
Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mlandu wa mtonzo wanga wochokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wake pa choipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala choipa chake. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigaile, zakuti amtengere akhale mkazi wake.