Ndipo panali nthawi yomweyo, Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m'zonse uzichita iwe;
1 Samueli 24:22 - Buku Lopatulika Ndipo Davide analumbirira Saulo. Saulo namuka kwao; koma Davide ndi anthu ake anakwera kunka kungaka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide analumbirira Saulo. Saulo namuka kwao; koma Davide ndi anthu ake anakwera kunka kungaka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide adalumbira zonsezi Saulo alikumva. Tsono Saulo adabwerera kwao, koma Davide ndi anthu ake adapitanso kuphanga kobisalira kuja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Davide analumbira pamaso pa Sauli. Pambuyo pake Sauli anabwerera kwawo, koma Davide ndi anthu ake anapitanso ku phanga kuja. |
Ndipo panali nthawi yomweyo, Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m'zonse uzichita iwe;
tsopano iwe undilumbirire ine pano pa Mulungu kuti sudzandinyenga ine, kapena mwana wanga, kapena mdzukulu wanga: koma monga ufulu ndakuchitira iwe udzandichitire ine, ndi dziko lomwe wakhalamo, ngati mlendo.
Mutipatse ana ake aamuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapachika kwa Yehova mu Gibea wa Saulo, wosankhika wa Yehova. Mfumu niti, Ndidzawapereka.
Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.
Pomwepo Saulo anati kwa Davide, Udalitsike iwe, mwana wanga Davide; udzachita ndithu champhamvu, nudzapambana. Chomwecho Davide anamuka, ndipo Saulo anabwera kwao.