1 Samueli 24:20 - Buku Lopatulika Ndipo tsono taona ndidziwa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndi kuti ufumu wa Israele udzakhazikika m'dzanja lako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsono taona ndidziwa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndi kuti ufumu wa Israele udzakhazikika m'dzanja lako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ona tsono, ndikudziŵa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndipo kuti ufumu wa Israele udzakhazikika pa iwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ona tsono, Ine ndikudziwa kuti udzakhala mfumu ndithu ndipo ufumu wa Israeli udzakhazikika mʼmanja mwako. |
mdani alondole moyo wanga, naupeze; naupondereze pansi moyo wanga, naukhalitse ulemu wanga m'fumbi.
Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.
Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.
Yehova akubwezere ntchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israele, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ake.
Koma tsopano ufumu wanu sudzakhala chikhalire; Yehova wadzifunira munthu wa pamtima pake; ndipo Yehova wamuika iye akhale mtsogoleri wa anthu ake, chifukwa inu simunasunge chimene Yehova anakulamulirani.
Ndipo iye ananena naye, Usaopa; chifukwa dzanja la Saulo atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Israele, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, ichinso Saulo atate wanga achidziwa.
Pomwepo Saulo anati kwa Davide, Udalitsike iwe, mwana wanga Davide; udzachita ndithu champhamvu, nudzapambana. Chomwecho Davide anamuka, ndipo Saulo anabwera kwao.