Ndipo Yuda anavomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, chifukwa ine sindinampatse iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwenso mkaziyo.
1 Samueli 24:17 - Buku Lopatulika Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adauza Davide kuti, “Iwe wachita chilungamo kupambana ine, pakuti wandichitira ine zabwino pamene ine ndakuchita zoipa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anawuza Davide kuti, “Ndiwe wolungama kuposa ine. Iwe wandikomera mtima pamene ine ndakuchitira zoyipa. |
Ndipo Yuda anavomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, chifukwa ine sindinampatse iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwenso mkaziyo.
Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndachimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa.
nanena, Ndinachita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tili nacho chiyani ife? Udzionere wekha.
Ndipo Saulo anazindikira mau ake a Davide, nati, Ndi mau ako awa, mwana wanga Davide? Nati Davide, Ndi mau anga mfumu, mbuye wanga.
Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.