Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.
1 Samueli 24:16 - Buku Lopatulika Ndipo kunali, pakutsiriza Davide kulankhula mau awa kwa Saulo, Saulo anati, Ndiwo mau ako kodi, mwana wanga Davide? Saulo nakweza mau ake, nalira misozi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali, pakutsiriza Davide kulankhula mau awa kwa Saulo, Saulo anati, Ndiwo mau ako kodi, mwana wanga Davide? Saulo nakweza mau ake, nalira misozi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide atamaliza kulankhula mau ameneŵa, Saulo adafunsa kuti, “Kani liwu limeneli ndi lakodi, mwana wanga Davide?” Apo Saulo adayamba kulira mokweza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide atatsiriza kuyankhula mawu awa, Sauli anafunsa kuti, “Kodi mawu amenewa ndi akodi mwana wanga Davide?” Sauli anayamba kulira mokweza. |
Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.
Tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri ku ntchito yake yonse.
Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pake, nampsompsona; ndipo analira iwo.
Pamenepo mzimu unavala Amasai, ndiye wamkulu wa makumi atatuwo, nati iye, Ndife anu, Davide, tivomerezana nanu mwana wa Yese inu: mtendere, mtendere ukhale ndi inu, ndi mtendere ukhale ndi athandizi anu; pakuti Mulungu wanu akuthandizani. Ndipo Davide anawalandira, nawaika akulu a magulu.
Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.
Potero sindinakuchimwirani ine, koma mundichitira choipa ndinu kundithira nkhondo; Yehova Woweruzayo, aweruze lero lino pakati pa ana a Israele ndi ana a Amoni.
Ndipo Saulo anazindikira mau ake a Davide, nati, Ndi mau ako awa, mwana wanga Davide? Nati Davide, Ndi mau anga mfumu, mbuye wanga.
Ndipo onani, monga lero ndinasamalira ndithu moyo wanu, momwemo usamaliridwe ndithu moyo wanga pamaso pa Yehova, ndipo Iye andipulumutse ku masautso onse.