Motero mfumu Yowasi sanakumbukire zokoma anamchitirazi Yehoyada atate wake, koma anapha mwana wake; ndiye pomwalira anati, Yehova achipenye, nachifunse.
1 Samueli 24:15 - Buku Lopatulika Chifukwa chake Yehova akhale woweruza, naweruze pakati pa ine ndi inu, nayang'anire, nandigwirire moyo, nandipulumutse m'dzanja lanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake Yehova akhale woweruza, naweruze pakati pa ine ndi inu, nayang'anire, nandigwirire moyo, nandipulumutse m'dzanja lanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake Chauta aweruze, ndipo agamule pakati pa ine ndi inu kupeza wolakwa. Anditeteze. Aonetse kulungama kwanga pondipulumutsa kwa inu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake Yehova agamule, inde aweruze pakati pa inu ndi ine ndi kupeza wolakwa. Yehova anditeteze ndi kundipulumutsa mʼdzanja lanu.” |
Motero mfumu Yowasi sanakumbukire zokoma anamchitirazi Yehoyada atate wake, koma anapha mwana wake; ndiye pomwalira anati, Yehova achipenye, nachifunse.
Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.
Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye mu Kachisi wake wopatulika.
Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndamchimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditulutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya chilungamo chake.
Potero sindinakuchimwirani ine, koma mundichitira choipa ndinu kundithira nkhondo; Yehova Woweruzayo, aweruze lero lino pakati pa ana a Israele ndi ana a Amoni.
Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine galu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide natchula milungu yake.
Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mlandu wa mtonzo wanga wochokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wake pa choipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala choipa chake. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigaile, zakuti amtengere akhale mkazi wake.
Chifukwa chake tsono, mwazi wanga usagwe pansi kutali ndi Yehova; pakuti mfumu ya Israele yatuluka kudzafuna nsabwe, monga munthu wosaka nkhwali pamapiri.