Ndipo mfumu inanena ndi Abiyatara wansembeyo, Pita ku Anatoti ku minda yako; pakuti wakutidwa ndi imfa; koma sindikupha iwe lero lino, chifukwa unanyamula likasa la Ambuye Yehova pamaso pa Davide atate wanga, ndi popeza unanzunzidwa monse umo atate wanga Davide anazunzidwamo.
ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wake wa Ikabodi, mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wovala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwe kuti Yonatani wachoka.
Chomwecho Davide ndi anthu ake anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri. Motero Davide analanditsa okhala mu Keila.