Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala mu Hazazoni-Tamara.
1 Samueli 23:29 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anakwera kuchokera kumeneko, nakhala m'ngaka za Engedi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anakwera kuchokera kumeneko, nakhala m'ngaka za Engedi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide adachoka kumeneko, nakhala m'mapanga a ku Engedi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Davide anachoka kumeneko ndi kukakhala ku mapanga a ku Eni Gedi. |
Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala mu Hazazoni-Tamara.
Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukulu wa anthu ochokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni-Tamara, ndiwo Engedi.
Wokondedwa wanga ali kwa ine ngati chipukutu cha maluwa ofiira m'minda yamipesa ya ku Engedi.
Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za mu Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.
ndi Nibisani, ndi Mzinda wa Mchere, ndi Engedi; mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao.
Chomwecho Saulo anabwerera polondola Davide, nakakomana ndi Afilisti; chifukwa chake anatchula dzina lake la malo aja, Thanthwe lolekanitsa.
Ndipo kunali, pakubwerera Saulo potsata Afilisti, anamuuza, kuti, Taonani, Davide ali ku chipululu cha Engedi.
Ndipo Davide analumbirira Saulo. Saulo namuka kwao; koma Davide ndi anthu ake anakwera kunka kungaka.