Ndipo anati, Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi Mpulumutsi wanga, wangadi.
1 Samueli 23:25 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo ndi anthu ake anamuka kukamfuna. Koma wina anauza Davide; chifukwa chake anatsikira kuthanthweko, nakhala m'chipululu cha Maoni. Ndipo pamene Saulo anamva ichi, iye anamlondola Davide m'chipululu cha Maoni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo ndi anthu ake anamuka kukamfuna. Koma wina anauza Davide; chifukwa chake anatsikira kuthanthweko, nakhala m'chipululu cha Maoni. Ndipo pamene Saulo anamva ichi, iye anamlondola Davide m'chipululu cha Maoni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Saulo ndi anthu ake adapita kukamfunafuna Davide, koma iye anali atazimva. Nchifukwa chake adathaŵa napita ku thanthwe la ku chipululu cha Maoni. Saulo atamva kuti Davide adathaŵira ku Maoni, adamlondola kuchipululu komweko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli ndi anthu ake anapita kukamufufuza Davide. Koma Davide atamva izi anathawa ndi kukabisala ku thanthwe la chipululu cha Maoni. Sauli atamva kuti Davide anathawira ku Maoni anamutsatira ku chipululu komweko. |
Ndipo anati, Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi Mpulumutsi wanga, wangadi.
Ndipo anawakantha nyung'unyu ndi ntchafu, makanthidwe aakulu; natsika nakhala m'phanga mwa thanthwe la ku Etamu.
Ndipo iwo ananyamuka, namuka ku Zifi asanapiteko Saulo; koma Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni, m'chigwa cha kumwera kwa chipululu.
Ndipo Saulo anamuka mbali ina ya phiri, Davide ndi anthu ake kuseri kwake; ndipo Davide anafulumira kuthawa, chifukwa cha kuopa Saulo; popeza Saulo ndi anthu ake anazinga Davide ndi anthu ake kwete kuti awagwire.
Chomwecho Saulo anabwerera polondola Davide, nakakomana ndi Afilisti; chifukwa chake anatchula dzina lake la malo aja, Thanthwe lolekanitsa.