1 Samueli 23:24 - Buku Lopatulika Ndipo iwo ananyamuka, namuka ku Zifi asanapiteko Saulo; koma Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni, m'chigwa cha kumwera kwa chipululu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo ananyamuka, namuka ku Zifi asanapiteko Saulo; koma Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni, m'chigwa cha kumwera kwa chipululu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthuwo adabwerera ku Zifi, Saulo asananyamuke. Pa nthaŵiyo Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni ku Araba, kumwera kwa Yesimoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero iwo ananyamuka ndi kupita ku Zifi, koma Sauli asananyamuke. Nthawi imeneyi Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni, ku Araba kummwera kwa Yesimoni. |
Chifukwa chake yang'anirani, ndi kudziwa ngaka zonse alikubisalamo iye, nimubwere kwa ine ndi mau otsimikizika, pomwepo ndidzamuka nanu; ndipo akakhala m'dzikomo, ndidzampwaira pakati pa mabanja onse a Yuda.
Ndipo Saulo ndi anthu ake anamuka kukamfuna. Koma wina anauza Davide; chifukwa chake anatsikira kuthanthweko, nakhala m'chipululu cha Maoni. Ndipo pamene Saulo anamva ichi, iye anamlondola Davide m'chipululu cha Maoni.
Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wake anali ku Karimele; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi chikwi chimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zake ku Karimele.