Onani, tsopanoli alikubisala kudzenje kapena kwina; ndipo kudzali poyamba kugwa ena, aliyense wakumva adzanena, Alikuphedwa anthu otsata Abisalomu.
1 Samueli 23:22 - Buku Lopatulika Mukanitu kuti mukadziwitse ndithu, ndi kudziwa ndi kuona mbuto m'mene akhalitsa, ndi amene adamuona m'menemo; chifukwa anandiuza kuti iye achita mochenjera ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mukanitu kuti mukadziwitse ndithu, ndi kudziwa ndi kuona mbuto m'mene akhalitsa, ndi amene adamuona m'menemo; chifukwa anandiuza kuti iye achita mochenjera ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pitani mukaonetsetse. Mukafufuze kumene kuli mbuto yake, ndi kupeza munthu amene wamuwona chamaso kumeneko. Ndikumva kuti ngwochenjera mwaukapsala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pitani mukatsimikizire. Mukaone kumene amakhala ndiponso mupeze munthu amene wamuona. Anthu amandiwuza kuti ndi wochenjera kwambiri. |
Onani, tsopanoli alikubisala kudzenje kapena kwina; ndipo kudzali poyamba kugwa ena, aliyense wakumva adzanena, Alikuphedwa anthu otsata Abisalomu.
Nati iye, Kamuoneni komwe ali; ndikatume munthu kumtenga. Ndipo anamuuza kuti, Ali ku Dotani.
Chifukwa chake yang'anirani, ndi kudziwa ngaka zonse alikubisalamo iye, nimubwere kwa ine ndi mau otsimikizika, pomwepo ndidzamuka nanu; ndipo akakhala m'dzikomo, ndidzampwaira pakati pa mabanja onse a Yuda.