1 Samueli 23:19 - Buku Lopatulika Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Saulo ku Gibea, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango ku Horesi, m'phiri la Hakila, limene lili kumwera kwa chipululu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Saulo ku Gibea, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango ku Horesi, m'phiri la Hakila, limene lili kumwera kwa chipululu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono anthu a ku Zifi adapita kwa Saulo ku Gibea, nakamuuza kuti, “Davide akubisala ku dera lakwathu m'mapanga a ku Horesi pa phiri la Hakila limene lili kumwera kwa Yesimoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ku Gibeya ndipo anamuwuza kuti, “Davide akubisala kwathu, mʼmapanga a ku Horesi, mʼphiri la Hakila, kummwera kwa Yesimoni. |
Ndipo kunali, pakubwerera Saulo potsata Afilisti, anamuuza, kuti, Taonani, Davide ali ku chipululu cha Engedi.
Ndipo Azifi anafika kwa Saulo ku Gibea, nati, Kodi Davide sali kubisala m'phiri la Hakila, kupenya kuchipululu!
Saulo namanga zithando m'phiri la Hakila kupenya kuchipululu kunjira. Koma Davide anakhala kuchipululu, naona kuti Saulo alikumfuna kuchipululu komweko.