Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.
1 Samueli 23:18 - Buku Lopatulika Ndipo awiriwo anapangana pangano pamaso pa Yehova; ndipo Davide anakhala kunkhalango, koma Yonatani anapita kunyumba yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo awiriwo anapangana pangano pamaso pa Yehova; ndipo Davide anakhala kunkhalango, koma Yonatani anapita kunyumba yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo aŵiriwo adachita chipangano pamaso pa Chauta. Choncho Davide adakhalabe ku Horesi, ndipo Yonatani adabwerera kwao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Awiriwa anachita pangano pamaso pa Yehova. Ndipo Yonatani anabwerera kwawo, koma Davide anakhalabe ku Horesi. |
Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.
Ndipo Davide anati, Kodi atsalako wina wa nyumba ya Saulo, kuti ndimchitire chifundo chifukwa cha Yonatani?
Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.
Pamenepo Yonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha.
Ndipo Yonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yako, nthawi zamuyaya. Ndipo iye ananyamuka nachoka; koma Yonatani anamuka kumzinda.
Chifukwa chake uchitire kapolo wako zokoma mtima; popeza wamchititsa kapolo wako kupangana nawe pangano la kwa Yehova; koma ngati mwa ine muli choipa chilichonse, undiphe wekha; udzapita nane bwanji kwa atate wako?
Ndipo Davide anafika ku Nobu kwa Ahimeleki wansembeyo; ndipo Ahimeleki anadza kukomana ndi Davide alikunjenjemera, nanena naye, Muli nokha bwanji, palibe munthu wina nanu?