1 Samueli 23:14 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anakhala m'chipululu m'ngaka, nakhala m'dziko la mapiri m'chipululu cha Zifi. Ndipo Saulo anamfunafuna masiku onse, koma Mulungu sadampereke m'dzanja lake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anakhala m'chipululu m'ngaka, nakhala m'dziko la mapiri m'chipululu cha Zifi. Ndipo Saulo anamfunafuna masiku onse, koma Mulungu sadampereka m'dzanja lake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide ankabisala m'mapanga m'dziko lamapiri ku chipululu cha Zifi. Monsemo Saulo ankamufunafuna, koma Mulungu sadalole kuti agwidwe ai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide ankakhala mʼmapanga mʼdziko lamapiri ku chipululu cha Zifi. Sauli ankamufufuza tsiku ndi tsiku, koma Mulungu sanapereke Davide mʼmanja mwake. |
Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.
Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.
Ndipo mfumu inauza Yerameele mwana wake wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Aziriele, ndi Selemiya mwana wa Abideele, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.
mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira mu Antiokeya, mu Ikonio, mu Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.
Ndipo Davide anaona kuti Saulo adatuluka kudzafuna moyo wake; Davide nakhala m'chipululu cha Zifi m'nkhalango ku Horesi.
Ndipo anthu anauza Saulo kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Saulo anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.
Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe choipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakuchimwirani, chinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire.
Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake.