Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamula likasa la chipangano la Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abiyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kutuluka m'mzindamo.
1 Samueli 22:20 - Buku Lopatulika Ndipo mmodzi wa ana a Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, dzina lake ndiye Abiyatara, anapulumuka, nathawira kwa Davide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mmodzi wa ana a Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, dzina lake ndiye Abiyatara, anapulumuka, nathawira kwa Davide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma mmodzi mwa ana aamuna a Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, dzina lake Abiyatara, adapulumuka, nathaŵa kutsatira Davide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Abiatara mwana wa Ahimeleki mwana wa Ahitubi anapulumuka ndi kuthawira kwa Davide. |
Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamula likasa la chipangano la Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abiyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kutuluka m'mzindamo.
Ndipo anapangana ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi Abiyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza.
Ndipo Davide anaitana Zadoki ndi Abiyatara ansembe, ndi Alevi Uriyele, Asaya, ndi Yowele, Semaya, ndi Eliyele, ndi Aminadabu, nanena nao,
Ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara, anali ansembe, ndi Savisa anali mlembi,
ndipo taonani, inadza mphepo yaikulu yochokera kuchipululu, niomba pangodya zonse zinai za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wake wa Ikabodi, mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wovala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwe kuti Yonatani wachoka.
Ndipo munthu wako, amene ndidzamleka osamlikha paguwa langa la nsembe, adzatha maso ako, ndi kumvetsa mtima wako chisoni; ndipo obadwa onse a m'banja lako adzamwalira akali biriwiri.
Ndipo kunali kuti Abiyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lake.
Ndipo Davide anadziwa kuti Saulo analikulingalira zomchitira zoipa; nati kwa Abiyatara wansembe, Bwera kuno ndi efodi.
Ndipo Davide ananena ndi Abiyatara wansembeyo, mwana wa Ahimeleki, Unditengere kuno efodi. Abiyatara nabwera ndi efodi kwa Davide.
Ndipo munthu wa fuko la Benjamini anathamanga kuchokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake.