Pamene mwamuna adzamgwira mbale wake m'nyumba ya atate wake, nadzati, Iwe uli ndi chovala, khala wolamulira wathu, ndi kupasula kumeneku kukhale m'dzanja lako;
1 Samueli 21:3 - Buku Lopatulika Chifukwa chake tsono muli ndi chiyani? Mundipatse m'dzanja langa mikate isanu, kapena chilichonse muli nacho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake tsono muli ndi chiyani? Mundipatse m'dzanja langa mikate isanu, kapena chilichonse muli nacho. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi muli ndi chakudya? Mundipatseko mitanda isanu yabuledi kapena chakudya chilichonse chimene muli nacho pano.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi muli ndi chakudya? Patseniko malofu a buledi asanu, kapena chilichonse muli nacho.” |
Pamene mwamuna adzamgwira mbale wake m'nyumba ya atate wake, nadzati, Iwe uli ndi chovala, khala wolamulira wathu, ndi kupasula kumeneku kukhale m'dzanja lako;
Mwenzi anthu awa akadakhala m'dzanja langa; ndikadamchotsadi Abimeleki. Ndipo anati kwa Abimeleki, Chulukitsa khamu lako, nutuluke.
Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira ntchito, ninena nane, Asadziwe munthu aliyense kanthu za ntchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.
Ndipo wansembeyo anayankha Davide nati, Ndilibe mkate wachabe, koma ulipo mkate wopatulika; pokhapo ngati anyamatawo anadzisunga kupewa akazi.