1 Samueli 21:15 - Buku Lopatulika Kodi ndisowa anthu amisala kuti mwabwera ndi uyu kuti akhale wamisala pamaso panga? Kodi uyu adzalowa m'nyumba mwanga? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi ndisowa anthu amisala kuti mwabwera ndi uyu kuti akhale wamisala pamaso panga? Kodi uyu adzalowa m'nyumba mwanga? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi ndikusoŵa anthu amisala kuti muzibwera naye kuno munthu ameneyu, namachita zamisala zake pamaso panga? Ha! Munthu wotereyu angaloŵe bwanji m'nyumba mwanga muno?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi ine ndikusowa anthu amisala kuti muzibwera naye munthuyu kwa ine kuti azidzachita zamisala zake pamaso panga? Kodi munthu ameneyu nʼkulowa mʼnyumba mwanga?” |
Tsono Akisi ananena ndi anyamata ake, Taonani, mupenya kuti munthuyo ngwa misala; mwabwera naye kwa ine chifukwa ninji?
Motero Davide anachoka kumeneko, napulumukira ku phanga la ku Adulamu; ndipo pamene abale ake ndi banja lonse la atate wake anamva, iwo anatsikira kumeneko kwa iye.