Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 21:14 - Buku Lopatulika

Tsono Akisi ananena ndi anyamata ake, Taonani, mupenya kuti munthuyo ngwa misala; mwabwera naye kwa ine chifukwa ninji?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Tsono Akisi ananena ndi anyamata ake, Taonani, mupenya kuti munthuyo ngwa misala; mwabwera naye kwa ine chifukwa ninji?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono Akisi adauza nduna zake kuti, “Mukuwona kuti munthuyu ngwamisala. Chifukwa chiyani tsono mwabwera naye kwa ine?

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Akisi anawuza nduna zake kuti, “Mukumuona munthu uyu kuti ndi wamisala! Nʼchifukwa chiyani mukubwera naye kwa ine?

Onani mutuwo



1 Samueli 21:14
4 Mawu Ofanana  

Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.


Indetu nsautso uyalutsa wanzeru; ndi mtulo uipitsa mtima.


Nasanduliza makhalidwe ake pamaso pao, nadzionetsera m'manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za chipata, nakhetsa dovu lake pa ndevu yake.


Kodi ndisowa anthu amisala kuti mwabwera ndi uyu kuti akhale wamisala pamaso panga? Kodi uyu adzalowa m'nyumba mwanga?