1 Samueli 21:13 - Buku Lopatulika Nasanduliza makhalidwe ake pamaso pao, nadzionetsera m'manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za chipata, nakhetsa dovu lake pa ndevu yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nasanduliza makhalidwe ake pamaso pao, nadzionetsera m'manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za chipata, nakhetsa dovu lake pa ndevu yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho adasintha khalidwe lake pamaso pao, nadzisandutsa ngati wamisala, namangolembalemba pa zitseko za chipata, malovu ali chuchuchu kutsikira ku ndevu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anasintha makhalidwe ake pamaso pawo, nʼkudzisandutsa ngati wamisala. Iye ankangolembalemba pa zitseko za chipata ndi kumangotuluka dovi, nʼkumayenderera mʼndevu zake. |
Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;
Ndipo pamene Saulo ndi Aisraele onse anamva mau ao a Mfilistiyo, anadodoma, naopa kwambiri.
Tsono Akisi ananena ndi anyamata ake, Taonani, mupenya kuti munthuyo ngwa misala; mwabwera naye kwa ine chifukwa ninji?