1 Samueli 20:40 - Buku Lopatulika Ndipo Yonatani anapatsa mnyamata wake zida zake, nanena naye, Muka, tenga izi kunka nazo kumzinda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yonatani anapatsa mnyamata wake zida zake, nanena naye, Muka, tenga izi kunka nazo kumudzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Yonatani adapereka zida zake kwa mnyamata wake uja, namuuza kuti, “Pita, kazitule ku mzinda.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pambuyo pake Yonatani anapereka zida zake za nkhondo kwa mnyamatayo ndipo anati, “Pita, nyamula ubwerere nazo ku mzinda.” |
Pomwepo pochoka mnyamatayo, Davide, anauka chakumwera, nagwa nkhope yake pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa.