Ndipo Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Yendetsa, fulumira, usaima. Ndi mnyamata wa Yonatani anatola mivi, nafika kwa mbuye wake.
1 Samueli 20:39 - Buku Lopatulika Koma mnyamatayo sanadziwe kanthu; Davide ndi Yonatani okha anadziwa za mlanduwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma mnyamatayo sanadziwe kanthu; Davide ndi Yonatani okha anadziwa za mlanduwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma mnyamatayo sadadziŵe kanthu ai, Yonatani yekha ndi Davide ndiwo amene ankadziŵa zimene zinkachitika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Mnyamatayo sanadziwe chimene chimachitika koma Yonatani ndi Davide ndiwo ankadziwa). |
Ndipo Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Yendetsa, fulumira, usaima. Ndi mnyamata wa Yonatani anatola mivi, nafika kwa mbuye wake.
Ndipo Yonatani anapatsa mnyamata wake zida zake, nanena naye, Muka, tenga izi kunka nazo kumzinda.