Ndipo mnyamatayo atafika pamalo a muvi umene Yonatani anauponya, Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Muviwo suli m'tsogolo mwako kodi?
1 Samueli 20:38 - Buku Lopatulika Ndipo Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Yendetsa, fulumira, usaima. Ndi mnyamata wa Yonatani anatola mivi, nafika kwa mbuye wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Yendetsa, fulumira, usaima. Ndi mnyamata wa Yonatani anatola mivi, nafika kwa mbuye wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yonatani adaitananso mnyamatayo nati, “Fulumira, yenda msanga, usachedwe.” Motero mnyamata uja adatola muviwo, nabwera kwa mbuyake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yonatani anayitananso mnyamatayo kuti, “Fulumira, pita msanga usayime.” Choncho mnyamatayo anatola muvi uja ndi kubwera nayo kwa mbuye wake. |
Ndipo mnyamatayo atafika pamalo a muvi umene Yonatani anauponya, Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Muviwo suli m'tsogolo mwako kodi?