Ndipo m'mawa, Yonatani ananka kuthengoko pa nthawi imene anapangana ndi Davide, ali ndi kamnyamata.
1 Samueli 20:36 - Buku Lopatulika Ndipo anauza mnyamata wakeyo, Thamanga uzikatola mivi imene ndidzaponya; ndipo analikuthamanga mnyamatayu, iye anaponya muvi kuutumphitsa iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anauza mnyamata wakeyo, Thamanga uzikatola mivi imene ndidzaponya; ndipo analikuthamanga mnyamatayu, iye anaponya muvi kuutumphitsa iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adauza mnyamata wake kuti, “Thamanga, ukatole mivi imene nditi ndiponye.” Mnyamata uja akuthamanga, Yonatani adaponya muvi patsogolo pa mnyamatayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono anawuza mnyamatayo kuti, “Thamanga ukatole muvi umene nditi ndiponye.” Mnyamatayo akuthamanga Yonatani anaponya muvi patsogolo pa mnyamatayo. |
Ndipo m'mawa, Yonatani ananka kuthengoko pa nthawi imene anapangana ndi Davide, ali ndi kamnyamata.