Ndipo anakwiya Yakobo namkalipira Labani: ndipo Yakobo anayankha nati kwa Labani, Kodi ndachimwa chiyani? Uchimo wanga nguti, kuti unanditsatatsata ine pambuyo panga?
1 Samueli 20:32 - Buku Lopatulika Ndipo Yonatani anayankha Saulo atate wake, nanena, Aphedwe chifukwa ninji? Anachitanji? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yonatani anayankha Saulo atate wake, nanena, Aphedwe chifukwa ninji? Anachitanji? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yonatani adafunsa bambo wake kuti, “Kodi chifukwa chiyani mufuna kumupha Davide? Kodi walakwa chiyani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yonatani anafunsa abambo ake kuti, “Nʼchifukwa chiyani mufuna kuti Davide aphedwe? Iye walakwa chiyani?” |
Ndipo anakwiya Yakobo namkalipira Labani: ndipo Yakobo anayankha nati kwa Labani, Kodi ndachimwa chiyani? Uchimo wanga nguti, kuti unanditsatatsata ine pambuyo panga?
Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.
Ndipo iye anati, Chifukwa ninji? Anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsa kopambana, Apachikidwe pamtanda.
Ndipo anati kwa iwo nthawi yachitatu, Nanga munthuyu anachita choipa chiyani? Sindinapeze chifukwa cha kufera Iye; chotero ndidzamkwapula Iye ndi kummasula.
Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene achita?
Ndipo Saulo anaponya mkondowo; pakuti anati, Ndidzapyoza Davide ndi kumphatikiza ndi khoma. Ndipo Davide analewa kawiri kuchoka pamaso pake.
Ndipo Yonatani analankhula ndi Saulo atate wake movomereza Davide, nanena naye, Mfumu asachimwire mnyamata wake Davide; chifukwa iyeyo sanachimwire inu, ndipo ntchito zake anakuchitirani zinali zabwino ndithu;
popeza iye anataya moyo wake nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anachitira Aisraele onse chipulumutso chachikulu, inu munachiona, nimunakondwera; tsono mudzachimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda chifukwa?
Ndipo Davide anathawa ku Nayoti mu Rama, nadzanena pamaso pa Yonatani, Ndachitanji ine? Kuipa kwanga kuli kotani? Ndi tchimo langa la pamaso pa atate wanu ndi chiyani, kuti amafuna moyo wanga?
Tsono akati, Chabwino; kapolo wako adzakhala ndi mtendere; koma akapsa mtima, uzindikirepo kuti anatsimikiza mtima kundichitira choipa.
Ndipo Ahimeleki anayankha mfumu, nati, Ndipo ndani mwa anyamata anu onse ali wokhulupirika ngati Davide amene, mkamwini wa mfumu; wakuyenda mu uphungu wanu, nalemekezeka m'nyumba mwanu?