Ndipo kunali tsiku lachiwiri mwezi utakhala, Davide adasowekanso pamalo pake; ndipo Saulo anati kwa Yonatani mwana wake, Mwana wa Yese walekeranji kubwera kudya dzulo ndi lero lomwe?
1 Samueli 20:28 - Buku Lopatulika Ndipo Yonatani anayankha Saulo, Davide anandiumiriza ndimlole amuke ku Betelehemu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yonatani anayankha Saulo, Davide anandiumiriza ndimlole amuke ku Betelehemu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yonatani adayankha kuti, “Davide adandipempha mondiwumiriza kuti ndimlole apite ku Betelehemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yonatani anayankha kuti, “Davide anandiwumiriza kuti ndimulole kuti apite ku Betelehemu. |
Ndipo kunali tsiku lachiwiri mwezi utakhala, Davide adasowekanso pamalo pake; ndipo Saulo anati kwa Yonatani mwana wake, Mwana wa Yese walekeranji kubwera kudya dzulo ndi lero lomwe?
nati, Ndiloleni, ndimuke; chifukwa banja lathu lipereka nsembe m'mzindamo; ndi mbale wanga anandiuzitsa ndifikeko; tsono ngati wandikomera mtima undilole ndichoke, ndikaone abale anga. Chifukwa cha ichi safika ku gome la mfumu.
Atate wako akandifuna pang'ono ponse, unene kuti, Davide anandiumirira ndimlole athamangire kwao ku Betelehemu, pakuti kumeneko kuli nsembe ya pachaka ya banja lao lonse.