Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samisoni. Nagalamuka iye m'tulo take, nati, Ndizituluka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwe kuti Yehova adamchokera.
1 Samueli 20:25 - Buku Lopatulika Mfumu nikhala pa mpando wake, monga ankachita nthawi zina, pa mpando wa pafupi pa khoma. Ndipo Yonatani anaimirira, ndi Abinere anakhala pa mbali ya Saulo; koma Davide anasoweka pamalo pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mfumu nikhala pa mpando wake, monga ankachita nthawi zina, pa mpando wa pafupi pa khoma. Ndipo Yonatani anaimirira, ndi Abinere anakhala pa mbali ya Saulo; koma Davide anasoweka pamalo pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adakhala pa mpando wake pafupi ndi khoma, monga m'mene ankachitira nthaŵi zonse. Yonatani adakhala popenyana naye, ndipo Abinere adakhala pambali pa mfumu Saulo, koma pa malo a Davide panalibe munthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anakhala pa malo ake a nthawi zonse pafupi ndi khoma moyangʼanana ndi Yonatani, ndipo Abineri anakhala moyandikana ndi Sauli, koma pa malo a Davide panalibe munthu. |
Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samisoni. Nagalamuka iye m'tulo take, nati, Ndizituluka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwe kuti Yehova adamchokera.
Tsono Yonatani ananena kwa Davide, Mawa mwezi ukhala; ndipo adzakufuna, popeza udzasoweka pamalo pako.
Chomwecho Davide anabisala kuthengo; ndipo pakukhala mwezi, mfumu inakhala pansi kudya.